18 Ndipo Zakariya anati kwa mngelo, Ndidzadziwitsa ici ndi ciani? Pakuti ndine nkhalamba, ndipo zaka zace za mkazi wanga zacuruka.
19 Ndipo mngelo anayankha, nati kwa iye, ine ndine Gabrieli, woimirira pamaso pa Mulungu; ndipo ndinatumidwa kwa iwe kudzalankhula nawe, ndi kuuza iwe uthenga uwu wabwino.
20 Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzacitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mau, anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yace.
21 Ndipo anthu analikulindira Zakariya, nazizwa ndi kucedwa kwace m'kacisimo.
22 Koma m'mene iye anaturukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kacisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.
23 Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wace anamarizidwa, anamuka kunyumba kwace.
24 Ndipo atatha masiku awa, Elisabeti mkazi wace anaima; nadzibisa miyezi isanu, nati,