15 Ndipo iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uli wonse; cifukwa moyo wace wa munthu sulingana ndi kucuruka kwa zinthu zace ali nazo.
16 Ndipo iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wace wa munthu mwini cuma unapatsa bwino.
17 Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndiribe mosungiramo zipatso zanga?
18 Ndipo anati, Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikuru, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi cuma canga.
19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli naco cuma cambiri cosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.
20 Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?
21 Atero iye wakudziunjikira cuma mwini yekha wosakhala naco cuma ca kwa Mulungu,