35 Khalani odzimangira m'cuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;
36 ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kucokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.
37 Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m'cuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.
38 Ndipo akadza ulonda waciwiri, kapena wacitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.
39 Koma zindikirani ici, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yace yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yace ibooledwe.
40 Khalani okonzeka inunso; cifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa munthu akudza.
41 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?