12 Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza cakudya ca pausana kapena ca madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a pfuko lako, kapena anansi ako eni cuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.
13 Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;
14 ndipo udzakhala wodala; cifukwa iwo alibe cakubwezera iwe mphotho; pakuti idzabwezedwa mphotho pa kuuka kwa oiungama.
15 Ndipo pamene wina wa iwo akuseama pacakudya pamodzi ndi iye anamva izi, anati kwa iye, Wodala iye amene adzadya mkate mu Ufumu wa Mulungu.
16 Koma anati kwa iye, Munthu wina anakonza phwando lalikuru; naitana anthu ambiri;
17 ndipo anatumiza kapolo wace pa nthawi ya phwando kukanena kwa oitanidwawo, idzani, cifukwa zonse zakonzeka tsopano.
18 Ndipo onse ndi mtima umodzi anayamba kuwiringula. Woyamba anati kwa iye, Ine ndagula munda, ndipo ndiyenera ndituruke kukauona; ndikupempha undilole ine ndisafika.