25 Ndipo mipingo yambiri ya anthu inamuka naye; ndipo iye anapotoloka, nati kwa iwo.
26 Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wace ndi amace, ndi mkazi wace, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ace, inde ndi moyo wace womwe wa iye mwini, sakhoza kukhala wophunzira wanga.
27 Ndipo amene ali yense sasenza mtanda wace wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sakhoza kukhala wophunzira wanga,
28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wace, aone ngati ali nazo zakuimariza?
29 Kuti kungacitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ace, osakhoza kuimariza, anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye,
30 ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumariza.
31 Kapena mfumu yanji pakupita kukomana ndi nkhondo ya mfumu inzace, sathanga wakhala pansi, nafunsana ndi akuru ngati akhoza ndi asilikari ace zikwi khumi kulimbana naye wina uja alikudza kukomana naye ndi asilikari zikwi makumi awiri?