20 Ndipo iye ananyamuka, nadza kwa atate wace. Koma pakudza iye kutali, atate wace anamuona, nagwidwa cifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pace, nampsompsonetsa.
21 Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinacimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kuchulidwa mwana wanu.
22 Koma atateyo ananena kwaakapolo ace, Turutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumbveke; ndipo mpatseni phete ku dzanja lace ndi nsapato ku apazi ace;
23 ndipo idzani naye mwana wa ng'ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere;
24 cifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa. Ndipo anayamba kusekera.
25 Koma mwana wace wamkuru anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuyimba ndi kubvina.
26 Ndipo anaitana mmodzi wa anayamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani?