1 Ndipo iye ananenanso kwa ophunzira ace, Panali munthu mwini cuma, anali ndi kapitao wace; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza cuma cace.
2 Ndipo anamuitana, nati kwa iye, ici ndi ciani ndikumva za iwe? Undiwerengere za ukapitao wako; pakuti sungathe kukhalabe kapitao.
3 Ndipo kapitao uyu anati mumtima mwace, Ndidzacita ciani, cifukwa mbuye wanga andicotsera ukapitao? kulima ndiribe mphamvu, kupemphapempha kundicititsa manyazi.
4 Ndidziwa cimene ndidzacita, kotero kuti pamene ananditurutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao.
5 Ndipo anadziitanira mmodzi ndi mmodzi amangawa onse a mbuye wace, nanena kwa woyamba, Unakongola ciani kwa mbuye wanga?
6 Ndipo anati, Mitsuko ya mafuta zana. Ndipo iye ananena naye, Tenga kalata wako, nukhale pansi msanga, nulembere, Makumi asanu.
7 Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Mitanga ya tirigu zana iye ananena naye, Tenga kalata wako nulembere makumi asanu ndi atatu.