8 Ndipo mbuye wace anatama kapitao wonyengayo, kuti anacita mwanzeru; cifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.
9 Ndipo Ine ndinena kwa inu, Mudziyesere nokha abwenzi ndi cuma cosalungama; kuti pamene cikakusowani, iwo akalandire inu m'mahema osatha.
10 Iye amene akhulupirika m'cacing'onong'ono alinso wokhulupirika m'cacikuru; ndipo iye amene ali wosalungama m'cacing'onong'ono alinso wosalungama m'cacikuru.
11 Cifukwa cace ngati simunakhala okhulupirika m'cuma ca cosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi cuma coona?
12 Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zace za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?
13 Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Cuma.
14 Koma Marisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.