1 Ndipo anati kwa ophunzira ace, Sikutheka kuti zolakwitsa zisadze; koma tsoka iye amene adza nazo.
2 Kukolowekedwa mwala wamphero m'khosi mwace ndi kuponyedwa Iye m'nyanja nkwapafupi, koma kulakwitsa mmodzi wa ang'ono awa nkwapatali.
3 Kadzicenjerani nokha; akacimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire.
4 Ndipo akakucimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lace, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.