17 Indetu ndinena kwa inu, Ali yense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati mwana, sadzalowamo ndithu.
18 Ndipo mkuru wina anamfunsa iye, nanena, Mphunzitsi wabwino, ndizicita ciani, kuti ndilowe moyo wosatha?
19 Koma Yesu anati kwa iye, Undicha Ine wabwino bwanji? palibe wabwino, koma mmodzi, ndiye Mulungu.
20 Udziwa malamulo. Usacite cigololo, Usaphe, Usabe, Usacite umboni wonama, Lemekeza atate wako ndi amako.
21 Koma anati, Izi zonse ndazisunga kuyambira ubwana wanga.
22 Koma m'mene Yesu anamva, anati kwa iye, Usowa cinthu cimodzi: gulitsa ziri zonse uli nazo, nugawire osauka; ndipo udzakhala naco cuma ceni ceni m'Mwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate Ine.
23 Koma pakumva izi anagwidwa naco cisoni cambiri; pakuti anali mwini cuma cambiri.