16 Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye ndalama yanu inacita nionjeza ndalama khumi.
17 Ndipo anati kwa iye, Cabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'cacing'onong'ono, khala nao ulamuliro pa midzi khumi.
18 Ndipo anadza waciwiri, nanena, Mbuye, ndalama yanu yapindula ndalama zisanu.
19 Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza midzi isanu.
20 Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi ndalama yanu, ndaisunga m'kansaru;
21 pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula cimene simunaciika pansi, mututa cimene simunacifesa.
22 Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula cimene sindinaciika, ndi wotuta cimene sindinacifesa;