3 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Ndidzakufunsani mau Inenso; mundiuze:
4 Ubatizo wa Yohane unacokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu?
5 Ndipo anatsutsana mwa okha, nanena, Ngati tinena ucokera Kumwamba; adzati, Simunamkhulupirira cifukwa ninji?
6 ndiponso, tikanena, Ucokera kwa anthu; anthu onse adzatiponya miyala: pakuti akopeka mtima, kuti Yohane ali mneneri.
7 Ndipo anayankha kuti sadziwa kumene ucokera.
8 Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ndingakhale Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndicita nao zinthu izi.
9 Ndipo iye anayamba kunena kwa anthu fanizo ili: Munthu analima munda wamphesa, naukongoletsa kwa olima munda, nanka ku dziko lina, nagonerako nthawi yaikuru.