2 Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri.
3 Ndipo iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse;
4 pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwace anaikamo za moyo wace, zonse anali nazo.
5 Ndipo pamene ena analikunena za Kacisiyo, kuti anakonzeka ndi miyala yokoma ndi zopereka, anati iye,
6 Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzace, umene sudzagwetsedwa.
7 Ndipo iwo anamfunsa iye, nati, Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? ndipo cizindikilo ndi cianipamene izi ziti zicitike?
8 Ndipo iye anati, Yang'anirani musasoceretsedwe; pakuti ambiri adzadza m'dzina langa, nadzanena, Ndine amene; ndipo, Nthawi yayandikira; musawatsate pambuyo pao.