5 Ndipo anakondwera, napangana naye kumpatsa ndalama.
6 Ndipo iye anabvomera, nafunafuna nthawi yabwino yakumpereka iye kwa iwo, pakalibe khamu la anthu.
7 Ndipo tsiku la mikate yopanda cotupitsa linafika, limene inayenera kuphedwa nsembe ya Paskha.
8 Ndipo iye anatumiza Petro ndi Yohane, nati, Pitanimutikonzere ife Paskha, kuti tidye.
9 Ndipo iwo ananena naye, Mufuna tikakonzere kuti?
10 Ndipo iye anati kwa iwo, Onani, mutalowa m'mudzi, adzakomana ndinu munthu alikusenza mtsuko wa madzi; mumtsate ameneyo kunyumba kumene akalowako iye.
11 Ndipo mukanene kwa mwini nyumbayo, Mphunzitsi anena nawe, Cipinda ca alendo ciri kuti, m'mene ndikadye Paskha pamodzi ndi ophunzira anga?