10 Ndipo pamene anaunguza-unguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako, Ndipo iye anatero, ndi dzanja lace lina; bwerera momwe.
11 Koma iwowo anagwidwa misala; nalankhulana wina ndi mnzace kuti amcitire Yesu ciani.
12 Ndipo kunali masiku awa, iye anaturuka nanka kuphiri kukapemphera; nacezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.
13 Ndipo kutaca, anaitana ophunzira ace; nasankha mwa iwo khumi ndi awiri, amene anawachanso dzina lao atumwi:
14 Simoni, amene anamuchanso Petro, ndi Andreya mbale wace, ndi Yakobo, ndi Yohane, ndi Filipo, ndi Bartolomeyo,
15 ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wochedwa Zelote,
16 ndi Yuda mwana wa Yakobo, ndi Yudase Isikariote, amene anali wompereka iye.