25 Tsoka inu okhuta tsopano! cifukwa mudzamva njala, Tsoka inu, akuseka tsopano! cifukwa mudzacita maliro ndi kulira misozi.
26 Tsoka inu, pamene anthu onse adzanenera inu zabwino! pakuti makolo ao anawatero momwemo ananeri onama.
27 Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; citirani zabwino iwo akuda inu,
28 dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akucitira inu cipongwe.
29 Iye amene akupanda iwe pa tsaya limodzi umpatsenso linzace; ndi iye amene alanda copfunda cako, usamkanize malaya ako.
30 Munthu ali yense akakupempha kanthu, umpatse; ndi iye amene alanda zako, usazipemphanso.
31 Ndipo monga mufuna inu kuti anthu adzakucitirani inu, muwacitire iwo motero inu momwe.