15 Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amace.
16 Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace.
17 Ndipo mbiri yace imeneyo inabuka ku Yudeya lonse, ndi ku dziko lonse loyandikira.
18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi.
19 Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ace, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
20 Ndipo pakufika kwa iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
21 Nthawi yomweyo iye anaciritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zobvuta, ndi mizimu yoipa; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.