20 Pomwepo Iye anayamba kutonza midziyo, m'mene zinacitidwa zambiri za nchito zamphamvu zace, cifukwa kuti siinatembenuke.
21 Tsoka kwa iwe, Korazini! tsoka kwa iwe, Betsaida! cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa inu zikadacitidwa m'Turo ndi m'Sidoni, akadatembenuka mtima kale kale m'ziguduli ndi m'phulusa.
22 Komanso ndinena kwa inu kuti dzuwa la kuweruza mlandu wao wa Turo ndi Sidoni udzacepa ndi wanu.
23 Ndipo iwe, Kapernao, udzakwezedwa kodi kufikira kuthambo? udzatsika kufikira ku dziko la akufa: cifukwa ngati zamphamvu zimene zacitidwa mwa iwe zikadacitidwa m'Sodomu, uyo ukadakhala kufikira lero.
24 Komanso ndinena kwa im kuti dzuwa la kuweruza, mlandu wace wa Sodomu udzacepa ndi wako.
25 Nyengo imeneyo Yesu anayankha nati, Ndibvomerezana ndi Inu, Atate, Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi, kuti munazibisira izo kwa anzeru ndi akudziwitsa, ndipo munaziululira zomwe kwa makanda:
26 etu, Atate, cifukwa cotero cinakhala cokondweretsa pamaso panu.