32 kamene kakhaladi kakang'ono koposa mbeu zonse, koma katakula, kali kakakuru kuposa zitsambazonse, nukhala mtengo, kotero kuti mbalame za mlengalenga zimadza, nizibindikira mu nthambi zace.
33 Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi cotupitsa mikate, cimene mkazi anacitenga, nacibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.
34 Zonsezi Yesu anaziphiphiritsira m'mafanizo kwa makamu anthu; ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo;
35 kuti cikacitidwe conenedwa ndi mneneri, kuti,Ndidzatsegula pakamwa panga ndi mafanizo;Ndidzaulula zinthu zobisika ciyambire kukhazikidwa kwace kwa dziko lapansi.
36 Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
37 Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa munthu;
38 ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;