36 Pomwepo Iye anasiya makamuwo, nalowa m'nyumba; ndimo ophunzira ace anadza kwa Iye, nanena, Mutitanthauzire fanizo lija la namsongole wa m'munda.
37 Ndipo Iye anayankha nati, Wofesa mbeu yabwino ndiye Mwana wa munthu;
38 ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbeu yabwino ndiyo ana a Ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo;
39 ndipo mdani amene anamfesa uwu ndiye mdierekezi: ndi kututa ndico cimariziro ca nthawi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.
40 Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, matero mudzakhala m'cimariziro ca nthawi ya pansi pano.
41 Mwana wa munthu adzatuma angelo ace, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kucotsa mu Ufumu wace zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akucita kusayeruzika,
42 ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.