24 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Inenso ndikufunsani mau amodzi, amene ngati muneliuza, Inenso ndikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi:
25 Ubatizo wa Yohane, ucokera kuti? Kumwamba kodi kapena kwa anthu? Koma iwo anafunsana wina ndi mnzace, kuti, Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye?
26 Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.
27 Ndipo anamyankha Yesu, nati, Sitidziwa ife. Iyenso ananena nao, lnenso sindikuuzani ndi ulamuliro wotani ndizicita izi.
28 Nanga mutani? Munthu anali cao ana awiri; nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero nchito ku munda wampesa.
29 Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pace analapa mtima napita.
30 Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anabvomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapita.