29 Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pace analapa mtima napita.
30 Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anabvomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapita.
31 Ndani wa awiriwo anacita cifuniro ca atate wace? Iwo ananena, Woyambayo. Yesu ananena kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi aciwerewere amatsogolera inu, kulowa mu Ufumu wa Kumwamba.
32 Popeza Yohane anadza kwa inu m'njira ya cilungamo, ndipo simunamveraiye; koma amisonkho ndi akazi aciwerewere anammvera iye; ndipo inu, m'mene munaciona, simunalapa pambuyo pace, kuti mumvere iye.
33 Mverani fanizo lina: Panali munthu, mwini banja, amene analima munda wamphesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mphesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina.
34 Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ace kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zace.
35 Ndipo olimawo anatenga akapolo ace, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala.