22 Ndipo pamene iwo anamva, anazizwa, namsiya Iye, nacokapo.
23 Tsiku lomwelo anadza kwa Iye Asaduki, amene amanena kuti palibe kuuka kwa akufa; namfunsa Iye,
24 nanena, Mphunzitsi, Mose anati, Ngati munthu akafa wopanda mwana, mphwace adzakwatira mkazi wace, nadzamuukitsira mbale wace mbeu.
25 Tsono panali ndi ife abale asanu ndi awiri; ndipo wakuyamba anakwatira, namwalira wopanda mbeu, nasiyira mphwace mkazi wace;
26 cimodzimodzi waciwiri, ndi wacitatu, kufikira wacisanu ndi ciwiri.
27 Ndipo pomarizira anamwaliranso mkaziyo.
28 Cifukwa cace m'kuuka kwa akufa, iye adzakhala mkazi wa yani wa asanu ndi awiriwo? pakuti onse anakhala naye.