39 Ndipo tinakuonani Inu liti wodwala, kapena m'nyumba yandende, ndipo tinadza kwa Inu?
40 Ndipo Mfumuyo idzayankha nidzati kwa iwo, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munacitira ici mmodzi wa abale anga, ngakhale ang'onong'ono awa, munandicitira ici Ine.
41 Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, Cokani kwa Ine otembereredwa inu, ku mota wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ace:
42 pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa Ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa Ine:
43 ndinali mlendo, ndipo simunandilandira Ine; wamarisece ndipo simunandibveka Ine; wodwala, ndi m'nyumba yandende, ndipo simunadza kundiona Ine.
44 Pomwepo iwonso adzayankha kuti, Ambuye, tinakuonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamarisece, kapena m'nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani Inu?
45 Pomwepo Iye adzayankha iwo kuti, Indetu ndinena kwa inu, Cifukwa munalibe kucitira ici mmodzi wa awa ang'onong'ono, munalibe kundicitira ici Ine.