18 Nati Iye, Mukani kumzinda kwa munthu wangana, mukati kwa iye, Mphunzitsi anena. Nthawi yanga yayandikirai ndidzadya Paskha kwanu pamodzi ndi ophunzira anga.
19 Ndipo ophunzira anacita monga Yesu anawauza, nakonza Paskha.
20 Ndipo pakufika madzulo, Iye analikukhala pacakudya pamodzi ndi ophunzira khumi ndi awiri;
21 ndipo m'mene analinkudya, Iye anati, Indetu ndinena kwa inu, mmodzi wa inu adzandipereka Ine.
22 Ndipo iwo anagwidwa ndi cisoni cacikuru, nayamba kunena kwa Iye mmodzi mmodzi, Kodi ndine, Ambuye?
23 Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lace m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine.
24 Mwana wa munthu acokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.