22 Ndipo iwo anagwidwa ndi cisoni cacikuru, nayamba kunena kwa Iye mmodzi mmodzi, Kodi ndine, Ambuye?
23 Ndipo Iye anayankha nati, Iye amene asunsa pamodzi ndi Ine dzanja lace m'mbale, yemweyu adzandipereka Ine.
24 Mwana wa munthu acokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa munthu aperekedwa ndi iye! kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.
25 Ndipo Yudase, womperekayo anayankha nati, Kedi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.
26 Ndipo pamene iwo analinkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo m'mene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani; ici ndi thupi langa.
27 Ndipo pamene anatenga cikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mumwere ici inu nonse,
28 pakuti ici ndici mwazi wanga wa pangano, wothiridwa cifukwa ca anthu ambiri ku kucotsa macimo.