52 Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Tabweza Iupanga lako m'cimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzaonongeka ndi Iupanga,
53 Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo Iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi awiri?
54 Koma pakutero malembo adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera comweco?
55 Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munaturukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wacifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala m'Kacisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira.
56 Koma izi zonse zinacitidwa, kuti 1 zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.
57 Ndipo iwo akugwira Yesu anaaka naye kwa Kayafa, mkuru wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akuru omwe.
58 Koma Petro anamtsata kutari, kufikira ku bwalo la mkuru wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone cimariziro.