57 Ndipo iwo akugwira Yesu anaaka naye kwa Kayafa, mkuru wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akuru omwe.
58 Koma Petro anamtsata kutari, kufikira ku bwalo la mkuru wa ansembe, nalowamo, nakhala pansi ndi anyamata, kuti aone cimariziro.
59 Ndipo ansembe akuru ndi akuru mirandu onse mafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;
60 koma sanaupeza zingakhale 2 mboni zonama zambiri zinadza. Koma pambuyo pace anadza awiri,
61 nati, Uyu ananena kuti, 3 Ndikhoza kupasula Kacisi, ndi kummanganso masiku atatu.
62 Ndipo mkuru wa ansembe anaimirira, nati kwa Iye, Subvomera kanthu kodi? nciani ici cimene awa akunenera Iwe?
63 Koma 4 Yesu anangokhala cete. Ndipo mkuru wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.