13 Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anaciritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
14 Ndipo pofika Yesu ku nyumba ya Petro, anaona mpongozi wace ali gone, alikudwala malungo.
15 Ndipo anamkhudza dzanja lace, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye.
16 Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa; ndipo Iye anaturutsa mizimuyo ndi mau, naciritsa akudwala onse;
17 kotero kuti cikwaniridwe conenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti,Iye yekha anatenga zofoka zathu,Nanyamula nthenda zathu.
18 Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke ku tsidya lina,
19 Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kuli konse mumukako.