8 Koma kenturiyoyo anabvomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzaciritsidwa mnyamata wanga.
9 Pakuti inenso ndiri munthu wakumvera ulamuliro, ndiri nao asilikari akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Cita ici, nacita.
10 Ndipo pakumva ici, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israyeli, sindinapeza cikhulupiriro cotere.
11 Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;
12 koma anawo a Ufumu adzatayidwa ku mdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.
13 Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anaciritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
14 Ndipo pofika Yesu ku nyumba ya Petro, anaona mpongozi wace ali gone, alikudwala malungo.