27 Abramu, (ndiye Abrahamu).
28 Ana a Abrahamu: Isake, ndi Ismayeli.
29 Mibadwo yao ndi awa; woyamba wa Ismayeli Nebayoti; ndi Kedara ndi Adibeli, ndi Mibisamu,
30 Misma, ndi Duma Masa,
31 Hadada, ndi Tema, Nafisi, ndi Kedema. Awa ndi ana a Ismayeli.
32 Ndi ana a Ketura mkazi wamng'ono wa Abrahamu anabala Zimiramu, ndi Yokisani, ndi Medani, ndi Midyani, ndi Isibaki, ndi Sua. Ndi ana a Yokisani: Seba, ndi Dedani.
33 Ndi ana a Midyani: Efa, ndi Eferi, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elidaa. Awa onse ndiwo ana a Ketura.