31 Hadada, ndi Tema, Nafisi, ndi Kedema. Awa ndi ana a Ismayeli.
32 Ndi ana a Ketura mkazi wamng'ono wa Abrahamu anabala Zimiramu, ndi Yokisani, ndi Medani, ndi Midyani, ndi Isibaki, ndi Sua. Ndi ana a Yokisani: Seba, ndi Dedani.
33 Ndi ana a Midyani: Efa, ndi Eferi, ndi Hanoki, ndi Abida, ndi Elidaa. Awa onse ndiwo ana a Ketura.
34 Ndipo Abrahamu anabala Isake. Ana a Isake: Esau, ndi Israyeli.
35 Ana a Esau: Elifazi, Reueli, ndi Yeuzi, ndi Yolamu, ndi Kora.
36 Ana a Elifazi: Teani, ndi Omara, Zefi, ndi Gatamu, Kenazi, ndi Timna, ndi Amaleki.
37 Ana a Reueli: Nahati, Zera, Sama, ndi Miza.