41 Mwana wa Ana: Disoni. Ndi ana a Disoni: Hamirani, ndi Esibani, ndi Itrani, ndi Kerani.
42 Ana a Ezeri: Bilani, ndi Zavani, ndi Yakani. Ana a Disani: Uzi, ndi Arani.
43 Mafumu tsono akucita ufumu m'dziko la Edomu, pakalibe mfumu wakucita ufumu pa ana a Israyeli, ndiwo Bela mwana wa Beori; ndi dzina la mudzi wace ndilo Dinaba.
44 Ndipo anafa Bela; ndi Yobabi mwana wa Zera wa ku Bozra anakhala mfumu m'malo mwace.
45 Namwalira Yobabi; ndi Husamu wa ku dziko la Atemani anakhala mfumu m'malo mwace.
46 Namwalira Husamu; ndi Hadada mwana wa Bedadi, amene anakantha Midyani ku thengo la Moabu, anakhala mfumu m'malo mwace; ndi dzina la mudzi wace ndi Aviti.
47 Namwalira Hadada; ndi Samla wa ku Masereka anakhala mfumu m'malo mwace.