18 Pamenepo mzimu unabvala Amasai, ndiye wamkuru wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tibvomerezana nanu mwana wa Jese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akuru a magulu.
19 Ena a Manase omwe anapambukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Sauli, koma sanawathandiza; popeza akalonga a Afilisti, atacita upo, anamuuza acoke, ndi kuti, Adzapambukira kwa mbuye wace Sauli ndi kutisandulikira.
20 Pomuka iye ku Zikilaga anapambukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yedyaeli, ndi Mikaeli, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akuru a zikwi a ku Manase.
21 Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la acifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.
22 Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikuru; ngati nkhondo ya Mulungu.
23 Ndipo kuwerenga kwa akuru okonzekeratu kunkhondo, anadzawo kwa Davide ku Hebroni, kupambukitsa ufumu wa Sauli ukhale wace, monga mwa mau a Yehova, ndi: uku.
24 Ana a Yuda akunyamula zikopa ndi mikondo ndiwo zikwi zisanu ndi cimodzi mphambu mazana asanu ndi atatu, okonzekeratu kunkhondo.