25 Pakuti Yehova ali wamkuru, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;Ayenera amuope koposa milungu yonse.
26 Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano;Koma Yehova analenga zakumwamba.
27 Pamaso pace pali ulemu ndi ukulu,M'malo mwace muli mphamvu ndi cimwemwe.
28 Mcitireni Yehova, inu mafuko a mitundu ya anthu,Mcitireni Yehova ulemerero ndi mphamvu.
29 Mcitireni Yehova ulemerero wa dzina lace;Bwerani naco copereka, ndipo fikani pamaso pace;Lambirani Yehova m'ciyero cokometsetsa,
30 Njenjemerani pamaso pace, inu dziko lonse lapansi,Dziko lokhalamo anthu lomwe lakhazikika, kuti silingagwedezeke.
31 Kukondwerere kumwamba, ndi dziko lapansi lisekerere;Anene mwa amitundu, Yehova acita ufumu.