3 Nagwira ali yense wa Israyeli, wamwamuna ndi wamkazi, yense mtanda wa mkate, ndi nthuli ya nyama, ndi ncinci ya mphesa zouma.
4 Ndipo anaika Alevi ena atumikire ku likasa la Yehova, nalalikire, nayamike, nalemekeze Yehova Mulungu wa Israyeli.
5 Asafu ndiye mkuru wao, ndi otsatana naye Zekariya, Yeieli, ndi Semiramoti, ndi Yehieli, ndi Matitiya, ndi Eliabu, ndi Benaya, ndi Obedi Edomu, ndi Yeieli, ndi zisakasa ndi azeze; koma Asafu ndi nsanje zomvekatu;
6 ndi Benaya ndi Yahazieli ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la cipangano la Mulungu.
7 Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.
8 Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.
9 Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.