6 ndi Benaya ndi Yahazieli ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la cipangano la Mulungu.
7 Tsiku limenelo tsono Davide anayamba kuwapatsa nyimbo ya kuyamika nayo Yehova; ocita ndiwo Asafu ndi abale ace.
8 Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.
9 Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.
10 Mudzitamandire ndi dzina lace lopatulika;Mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.
11 Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yace;Funani nkhope yace nthawi zonse.
12 Kumbukilani zodabwiza zace adazicita,Zizindikilo zace, ndi maweruzo a pakamwa pace;