8 Yamikani Yehova, itanani dzina lace;Bukitsani mwa mitundu ya anthu zocita iye.
9 Myimbireni, myimbireni zomlemekeza;Fotokozerani zodabwiza zace zonse.
10 Mudzitamandire ndi dzina lace lopatulika;Mitima yao ya iwo ofuna Yehova ikondwere.
11 Funsirani kwa Yehova ndi mphamvu yace;Funani nkhope yace nthawi zonse.
12 Kumbukilani zodabwiza zace adazicita,Zizindikilo zace, ndi maweruzo a pakamwa pace;
13 Inu mbeu ya Israyeli mtumiki wace,Inu ana a Yakobo, osankhika ace.
14 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;Maweruzo ace akhala pa dziko lonse lapansi,