1 Ndipo zitatha izi, Davide anakantha Afilisti, nawagonjetsa, nalanda Gati ndi midzi yace m'manja a Afilisti.
2 Anakanthanso Moabu; ndi Amoabu anakhala anthu a Davide, nabwera nazo mphatso,
3 Ndipo Davide anakantha Hadarezeri mfumu ya Zoba ku Hamati, pomuka iye kukhazikitsa ulamuliro wace ku mtsinje wa Firate.
4 Ndipo Davide analanda magareta ace cikwi cimodzi, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi oyenda pansi zikwi makumi awiri; Davide anadula mitsita akavalo onse okoka magareta, koma anasungako ofikira magareta zana limodzi.
5 Ndipo Aaramu a ku Damasiko anadza kudzathandiza Hadarezeri mfumu ya Zoba; koma Davide anakantha Aaramu amuna zikwi makumi awiri mphambu ziwiri.