1 Ana a Israyeli ndi awa: Rubeni, Simeoni, Levi, ndi Yuda, Isakara, ndi Zebuluni,
2 Dani, Yosefe, ndi Benjamini, Nafitali, Gadi, ndi Aseri.
3 Ana a Yuda ndiwo Eri, ndi Onani, ndi Sela; Batisua Mkanani anambalira atatu amenewa. Koma Eri mwana woyamba wa Yuda anali woipa pamaso pa Yehova, ndi iye anamupha.
4 Ndi Tamari mpongozi wace anambalira Perezi ndi Zera. Ana amuna onse a Yuda ndiwo asanu.
5 Ana a Perezi: Hezironi, ndi Hamuli.