14 Netaneli wacinai, Radai wacisanu,
15 Ozemu wacisanu ndi cimodzi, Davide wacisanu ndi ciwiri;
16 ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaili. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yoabu, ndi Asaheli; atatu.
17 Ndi Abigaili anabala Amasa; ndi atate wa Amasa ndiye Yeteri M-ismayeli.
18 Ndi Kalebi mwana wa Hezroni anabala ana ndi Azuba mkazi wace, ndi Yerioti; ndipo ana ace ndiwo Yeseri, ndi Sobabu, ndi Aridoni.
19 Namwalira Azuba, ndi Kalebi anadzitengera Efrati, amene anambalira Huri.
20 Ndi Huri anabala Uri, ndi Uri anabala Bezaleli.