24 Ndipo atafa Hezroni m'Kalebi-Efrata, Abiya mkazi wa Hezroni anambalira Asini atate wa Tekoa.
25 Ndi ana a Yerameli mwana woyamba wa Hezroni ndiwo: woyamba Ramu, ndi Buna, ndi Oreni, ndi Ozemu, ndi Ahiya.
26 Ndipo Yerameli anali naye mkazi wina dzina lace ndiye Atara, ndiye mace wa Onamu.
27 Ndipo ana a Ramu mwana woyamba wa Yerameli ndiwo Maazi, ndi Yamini, ndi Ekeri.
28 Ndi ana a Onamu ndiwo Samai, ndi Yada; ndi ana a Samai: Nadabu, ndi Abisuri.
29 Ndipo dzina la mkazi wa Abisuri ndiye Abihaili; ndipo anambalira Abani, ndi Molidi.
30 Ndi ana a Nadabu: Seledi ndi Apaimu; koma Seledi anamwalira wopanda ana.