40 ndi Eleasa anabala Sismai, ndi Sismai anabala Salumu,
41 ndi Salumu anabala Yekamiya, ndi Yekamiya anabala Elisama.
42 Ndi ana a Kalebi mbale wa Yerameli ndiwo Mesa mwana wace woyamba, ndiye atate wa Zifi; ndi ana a Maresa atate wa Hebroni.
43 Ndi ana a Hebroni: Kora, ndi Tapuwa, ndi Rekemu, ndi Sema.
44 Ndi Sema anabala Rahamu atate wa Yorikeamu, ndi Rekemu anabala Samai.
45 Ndi mwana wa Samai ndiye Maoni; ndipo Maoni ndiye atate wa Betizuri.
46 Ndi Efa mkazi wamng'ono wa Kalebi anabala Harani, ndi Moza, ndi Gazezi; ndi Harani anabala Gazezi.