50 Ana a Kalebi ndi awa: mwana wa Huri, mwana woyamba wa Efrata, Sobali atate wa Kiriate Yearimu.
51 Salma atate wa Betelehemu, Harefi atate wa Betigaderi.
52 Ndipo Sobali atate wa Kiriati-Yearimu anali ndi ana: Haroe, ndi Hazi Hamenukoti.
53 Ndi mabanja a Kiriati-Yearimu: Aitiri, ndi Aputi, ndi Asumati, ndi Amisrai; Aforati ndi Aestaoli anafuma kwa iwowa.
54 Ana a Salma: Betelehemu, ndi Anetofati, Atroti Beti Yoabu, ndi Hazi Hamanahati, ndi Azori.
55 Ndi mabanja a alembi okhala ku Yabezi: Atirati, Asimeati, Asukati. Iwo ndiwo Akeni ofuma ku Hamati, kholo la nyumba ya Rekabu.