31 Ndipo iwo aja Davide anawaimika a udindo wa nyimbo m'nyumba ya Yehova, litafikira kupumula likasalo, ndi awa.
32 Ndipo anatumikira ndi kuyimba pakhomo pa kacisi wa cihema cokomanako mpaka Solomo adamanga nyumba ya Yehova m'Yerusalemu, naimirira m'utumiki wao monga mwa malongosoledwe ao.
33 Ndipo oimirirawo, ndi ana ao, ndi awa: a ana a Akohati, Hemani woyimbayo, mwana wa Yoeli, mwana wa Samueli,
34 mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Elieli, mwana wa Towa,
35 mwana wa Zufi, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai,
36 mwana wa Elikana, mwana wa Yoeli, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya,
37 mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Abiasafu, mwana wa Kora,