44 Ndi ku dzanja lamanzere abale ao ana a Merari: Etani mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki,
45 mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya,
46 mwana wa Amzi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri,
47 mwana wa Mali, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi.
48 Ndi abale ao Alevi anaikidwa acite za utumiki ziti zonse za kacisi wa nyumba ya Mulungu.
49 Koma Aroni ndi ana ace adafofukiza pa guwa la nsembe yopsereza, ndi pa guwa la nsembe yofukiza, cifukwa ca nchito yonse ya malo opatulikitsa, ndi kucitira Israyeli cowatetezera, monga mwa zonse Mose mtumiki wa Mulungu adawauza.
50 Ndipo ana a Aroni ndiwo Eleazara mwana wace, Pinehasi mwana wace, Abisua mwana wace,