69 ndi Ayaloni ndi mabusa ace, ndi Gatirimoni ndi mabusa ace,
70 ndi motapa pa pfuko la Manase logawika pakati, Aneri ndi mabusa ace, ndi Bileamu ndi mabusa ace, kwa otsala a mabanja a ana a Kohati.
71 Ana a Gerisomu analandira motapa pa mabanja a pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndi Asitaroti ndi mabusa ace;
72 ndi motapa pa pfuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ace, Daberati ndi mabusa ace,
73 ndi Ramoti ndi mabusa ace, ndi Anemu ndi mabusa ace;
74 ndi motapa pa pfuko la Aseri, Masala ndi mabusa ace, ndi Abidoni ndi mabusa ace,
75 ndi Hukoki ndi mabusa ace, ndi Rehobu ndi mabusa ace;