71 Ana a Gerisomu analandira motapa pa mabanja a pfuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basana ndi mabusa ace, ndi Asitaroti ndi mabusa ace;
72 ndi motapa pa pfuko la Isakara, Kedesi ndi mabusa ace, Daberati ndi mabusa ace,
73 ndi Ramoti ndi mabusa ace, ndi Anemu ndi mabusa ace;
74 ndi motapa pa pfuko la Aseri, Masala ndi mabusa ace, ndi Abidoni ndi mabusa ace,
75 ndi Hukoki ndi mabusa ace, ndi Rehobu ndi mabusa ace;
76 ndi motapa pa pfuko la Nafitali, Kadesi m'Galileya ndi mabusa ace, ndi Hamoni ndi mabusa ace, ndi Kiriyataimu ndi mabusa ace.
77 Otsala a Alevi analandira, motapa pa pfuko la Zebuluni, Rimono ndi mabusa ace, Tabora ndi mabusa ace;