1 Ana a Isakara ndiwo Tola, ndi Pua, Yasubu ndi Simironi; anai.
2 Ndi ana a Tola: Uzi, ndi Repaya, ndi Yerieli, ndi Yamai, ndi Ibsamu, ndi Semueli, akuru a nyumba za makolo; ao ndiwo a Tola, ngwazi zamphamvu, m'mibadwo yao; kuwerenga kwao masiku a Davide ndiko zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi limodzi.
3 Ndi mwana wa Uzi: Izrahiya; ndi ana a Izrahiya: Mikaeli, ndi Obadiya, ndi Yoeli, ndi Isiya; onse asanuwa ndiwo akuru.
4 Ndi pamodzi nao mwa mibadwo yao, mwa nyumba za makolo ao, panali magulu a nkhondo zikwi makumi atatu mphambu zisanu ndi cimodzi, popeza anacuruka akazi ao ndi ana ao.