28 Ndipo dziko lao, ndi pokhala pao ndizo Beteli ndi miraga yace, ndi kum'mawa Narani, ndi kumadzulo Gezeri ndi miraga yace, ndi Sekemu ndi miraga yace, mpaka Aza ndi miraga yace;
29 ndi kumalire a ana a Manase; Beteseani ndi miraga yace, Taanaki ndi miraga yace, Megido ndi miraga yace, Dora ndi miraga yace. M'menemo anakhala ana a Yosefe mwana wa Israyeli.
30 Ana a Aseri: Imna, ndi Isva, ndi Isvi, ndi Beriya, ndi Sera mlongo wao.
31 Ndi ana a Beriya: Heberi, ndi Malikieli, ndiye atate wa Birizaiti.
32 Ndi Heberi anabala Yafteti, ndi Someri, ndi Hotamu, ndi Suwa mlongo wao.
33 Ndi ana a Yafteti: Pasaki, ndi Bimali, ndi Asvati. Awa ndi ana a Yafteti.
34 Ndi ana a Semeri: Ahi, ndi Roga, Yehuba, ndi Aramu.